Nehemiah 5:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo ndidaŵauza kuti, “Monga m'mene kwathekera, tayesetsa kuwombola abale athu, Ayuda amene adaagulitsidwa ngati akapolo kwa anthu a mitundu ina. Koma tsopano inu mukugulitsa ngakhale abale anu omwe kwa anzao, kuti ife tiwumirizidwe kuŵaombola.” Anthuwo adangokhala chete osaona ponena.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinanena nao, Ife monga umo tinakhoza, tinaombola abale athu Ayuda ogulitsidwa kwa amitundu; ndipo kodi inu mukuti mugulitse abale anu, kapena tiwagule ndi ife? Pamenepo anakhala duu, nasowa ponena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo ndinati, “Monga zakhaliramu ife tikutha kuwombola abale anthu amene anagulitsidwa ukapolo kwa anthu ena. Kodi tsopano inu mukugulitsanso abale anu kwa anzawo kuti ife tiwumirizidwe kuwawombola?” Iwo anakhala chete, chifukwa sanapeze mawu oti anene.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinanena, nao, Ife monga umo tinakhoza, tinaombola abale athu Ayuda ogulitsidwa kwa amitundu; ndipo kodi inu mukuti mugulitse abale anu, kapena tiwagule ndi ife? Pamenepo anakhala du, nasowa ponena.