Nehemiah 6:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kudangotero kuti Sanibalati, Tobiya, Gesemu Mwarabu ndiponso adani athu ena adamva kuti tidatha kumanganso khoma, ndipo kuti sipadatsale mpamodzi pomwe pogumuka, ngakhale tinali tisanaike zitseko pa zipata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kunali tsono, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Gesemu Mwarabu, ndi adani athu otsala, kuti ndidatha kumanga lingali, posatsalaponso popasuka; (ngakhale pajapo sindinaika zitseko pazipata);
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Sanibalati, Tobiya, Gesemu Mwarabu ndi adani athu anamva kuti ndatsiriza ntchito yomanganso khoma ndi kuti palibe mpata umene watsala ngakhale kuti pa nthawi imeneyi ndinali ndisanayike zitseko pa zipata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kunali tsono, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Gesemu M-arabu, ndi adani athu otsala, kuti ndidatha kumanga lingali, posatsalaponso popasuka; (ngakhale pajapo sindinaika zitseko pazipata);