Nehemiah 6:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo ndidapita ku nyumba ya Semaya, mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, amene sankatuluka m'nyumba mwake. Iye adandiwuza kuti, “Tiyeni tikabisale m'Nyumba ya Mulungu, tikatsekeko pakuti akubwera kudzakuphani. Ndithudi, akubwera usiku kudzakuphani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ndinalowa m'nyumba ya Semaya mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, wobindikizidwayo, ndipo anati, Tikomane kunyumba ya Mulungu m'kati mwa Kachisi, titsekenso pa makomo a Kachisi; pakuti akudza kudzapha iwe, inde akudza usiku kudzapha iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina ndinapita ku nyumba ya Semaya mwana wa Delaya mwana wa Mehatabeli. Tsono anandiwuza kuti, “Tiyeni tikakumanire ku Nyumba ya Mulungu. Tikabisale mʼmenemo ndi kutseka zitseko chifukwa akubwera kudzakuphani. Ndithu usiku uno akubwera kudzakuphani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ndinalowa m'nyumba ya Semaya mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, wobindikizidwayo, ndipo anati, Tikomane ku nyumba ya Mulungu m'kati mwa Kacisi, titsekenso pa makomo a Kacisi; pakuti akudza kudzapha iwe, inde akudza usiku kudzapha iwe.