Nehemiah 6:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ine ndidayankha kuti, “Munthu wonga ine nkuthaŵa kodi? Ndipo munthu wonga ine, kodi nkukabisala m'Nyumba ya Mulungu, kuti ndidzipulumutse? Zimenezo ai, toto, ine sindipitako!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndinati, Munthu ngati ine nkuthawa kodi? Ndani wonga ine adzalowa m'Kachisi kupulumutsa moyo wake? Sindidzalowamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndinayankha kuti, “Kodi munthu ngati ine nʼkuthawa? Kapena munthu wofanana ndi ine nʼkupita ku Nyumba ya Mulungu kuti apulumutse moyo wake? Ayi, ine sindipita!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndinati, Munthu ngati ine nkuthawa kodi? ndani wonga ine adzalowa m'Kacisi kupulumutsa moyo wace? sindidzalowamo.