Nehemiah 6:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimene adaamlembera ntchitoyo nkuti andichititse mantha, ineyo ndithaŵe. Motero ndikadachimwa, ndipo iwowo akadandiipitsira mbiri kuti azidzandinyodola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anamlembera chifukwa cha ichi, kuti ine ndichite mantha, ndi kuchita chotero, ndi kuchimwa; ndi kuti anditolerepo mbiri yoipa ndi kundinyoza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye analembedwa ntchitoyi ndi cholinga choti ine ndichite mantha, ndithawe. Ndikanatero ndiye kuti ndikanachimwira Yehova ndiponso iwowo akanandiyipitsira mbiri yanga ndi kumandinyoza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anamlembera cifukwa ca ici, kuti ine ndicite mantha, ndi kucita cotero, ndi kucimwa; ndi kuti anditolerepo mbiri yoipa ndi kundinyoza.