Nehemiah 6:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo ndidapemphera kuti, “Inu Mulungu wanga, kumbukirani zimene Tobiya ndi Sanibalati adachita. Kumbukiraninso zimene mneneri wamkazi Nowadiya ndiponso aneneri ena aja ankachita pofuna kundichititsa mantha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukumbukire, Mulungu wanga, Tobiya ndi Sanibalati monga mwa ntchito zao izi, ndi Nowadiya mneneri wamkazi yemwe, ndi aneneri otsala, amene anafuna kundiopsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ndinapemphera kuti, “Inu Mulungu wanga, kumbukirani Tobiya ndi Sanibalati chifukwa cha zimene achita. Kumbukiraninso mneneri wamkazi Nowadiya ndi aneneri amene akhala akufuna kundiopseza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukumbukile, Mulungu wanga, Tobiya ndi Sanibalati monga mwa nchito zao izi, ndi Nowadiya mneneri wamkazi yemwe, ndi aneneri otsala, amene anafuna kundiopsa.