Nehemiah 6:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adani athu onse a m'madera oyandikana nafe atamva zimenezi, adachita mantha kwambiri. Adachita manyazi pakuti iwo adaazindikira kuti ntchitoyo yachitika ndi chithandizo cha Mulungu wathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali atachimva adani athu onse, amitundu onse akutizinga anaopa, nagwadi nkhope; popeza anazindikira kuti ntchitoyi inachitika ndi Mulungu wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adani athu onse atamva izi, mitundu yonse ya anthu yozungulira inachita mantha ndi kuchita manyazi. Iwo anazindikira kuti ntchitoyo inachitika ndi thandizo la Mulungu wathu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali atacimva adani athu onse, amitundu onse akutizinga anaopa, nagwadi nkhope; popeza anazindikira kuti nchitoyi inacitika ndi Mulungu wathu.