Nehemiah 6:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pakuti anthu ambiri ku Yuda adaalumbira kuti adzagwirizana naye, chifukwa chakuti anali mkamwini wa Myuda mnzao, Sekaniya, mwana wa Ara. Ndipo mwana wake, Yehohanani, anali atakwatira mwana wamkazi wa Mesulamu, mwana wa Berekiya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ambiri m'Yuda analumbirirana naye chibwenzi; popeza ndiye mkamwini wake wa Sekaniya mwana wa Ara; ndi mwana wake Yehohanani adadzitengera mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pakuti anthu ambiri a ku Yuda anali atalumbira kale kuti adzagwira naye ntchito popeza anali mkamwini wa Sekaniya mwana wa Ara, ndipo mwana wake Yehohanani anakwatira mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ambiri m'Yuda analumbirirana naye cibwenzi; popeza ndiye mkamwini wace wa Sekaniya mwana wa Ara; ndi mwana wace Yehohanana adadzitengera mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya.