Nehemiah 6:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ankasimba za ntchito zabwino za Tobiyayo ine ndili pomwepo, ndipo ankamuululira mau anga. Choncho iyeyo ankalemba makalata ondichititsa mantha aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anatchulanso ntchito zake zokoma pamaso panga namfotokozera iye mau anga. Ndipo Tobiya anatumiza akalata kuti andiopse ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuwonjezera apo, anthu ankasimba za ntchito zake zabwino ine ndili pomwepo ndipo anakamuwululira mawu anga. Choncho Tobiyayo ankatumiza makalata ondiopseza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anachulanso nchito zace zokoma pamaso panga namfotokozera iye mau anga. Ndipo Tobiya anatumiza akalata kuti andiopse ine.