Nehemiah 6:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwaikanso aneneri ku Yerusalemu oti azilengeza za inu kuti, ‘Ku Yuda kuli mfumu tsopano!’ Tsono zonsezi zimveka ndithu kwa mfumu ya ku Persiya. Choncho mubwere kuti tidzakambirane tonse pamodzi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso waika aneneri akubukitsa za iwe ku Yerusalemu, ndi kuti, Ku Yuda kuli mfumu, ndipo zidzamveka kwa mfumu, kuti kuli zotere. Tiyeni tsono tipangane pamodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwayikanso kale aneneri amene adzalengeza za iwe mu Yerusalemu kuti ‘Mu Yuda muli mfumu!’ Tsono nkhani iyi imveka ndithu kwa mfumu. Choncho bwerani kuti tidzakambirane.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso waika aneneri akubukitsa za iwe ku Yerusalemu, ndi kuti, Ku Yuda kuli mfumu, ndipo zidzamveka kwa mfumu, kuti kuli zotere. Tiyeni tsono tipangane pamodzi.