Nehemiah 6:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaazindikira kuti adaniwo ankangofuna kutiwopsa, namaganiza kuti, “Ayudaŵa adzachita mantha ndipo adzaleka kugwira ntchito, motero ntchitoyo siidzatha.” Koma ine ndidapemphera kuti, “Inu Mulungu, tsopano mundilimbitse mtima.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja ao adzaleka ntchito, ndipo siidzachitika. Koma Inu, Mulungu, mulimbitse manja anga tsopano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Apa adani athu onsewa ankangofuna kutiopseza. Iwo ankaganiza kuti “Tichita mantha ndi kuleka kugwira ntchito.” Tsono ndinapemphera kuti, “Inu Mulungu ndilimbitseni mtima.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja ao adzaleka nchito, ndipo siidzacitika. Koma Inu, Mulungu, mulimbitse manja anga tsopano.