Nehemiah 7:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo ndidasankha mbale wanga Hanani ndi Hananiya, mkulu woyang'anira linga lankhondo, kuti aŵiriwo azilamulira Yerusalemu. Hananiyayo anali munthu wokhulupirika ndi womvera Mulungu kupambana anthu ambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndinawapatsa mbale wanga Hanani, ndi Hananiya kazembe wa kuboma, ulamuliro wa pa Yerusalemu; popeza ndiye munthu wokhulupirika, naposa ambiri pakuopa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndinawapatsa mbale wanga Hanani, ndi Hananiya kazembe wa kuboma, ulamuliro wa pa Yerusalemu; popeza ndiye munthu wokhulupirika, naposa ambiri pakuopa Mulungu.