Nehemiah 7:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndidaŵauza kuti, “Musalole kuti atsekule zipata za Yerusalemu mpaka dzuŵa litatentha. Ndipo atseke zitseko ndi kuzipiringidza, alonda asanaŵeruke. Musankhe olonda pakati pa anthu okhala m'Yerusalemu, aliyense akhale pamalo pake, ndiponso akhale poyang'anana ndi nyumba yake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinanenanso nao, Asatsegule pa zipata za Yerusalemu lisanafunde dzuwa; ndi poimirira odikira atseke pazipata, nimuzipiringidze, nimuike alonda mwa iwo okhala m'Yerusalemu, yense polindirira pake, yense pandunji pa nyumba yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinawawuza kuti, “Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinanenanso nao, Asatsegule pa zipata za Yerusalemu lisanafunde dzuwa; ndi poimirira odikira atseke pazipata, nimuzipiringidze, nimuike alonda mwa iwo okhala m'Yerusalemu, yense polindirira pace, yense pandunji pa nyumba yace.