Nehemiah 7:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu, koma anthu okhala mumzindamo anali oŵerengeka, ndipo munalibe nyumba zambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mudziwo tsono ndi wachitando, ndi waukulu; koma anthu anali m'mwemo ngowerengeka, nyumba zomwe sizinamangike.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mudziwo tsono ndi wacitando, ndi waukuru; koma anthu anali m'mwemo ngowerengeka, nyumba zomwe sizinamangike.