Nehemiah 7:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mulungu adaika mumtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse atsogoleri, akuluakulu ndiponso anthu onse, kuti alembedwe potsata mibadwo ya mabanja ao. Ndidapeza buku m'mene mudalembedwa maina a mabanja a anthu amene anali oyamba kubwerako ku ukapolo. Zolembedwa m'menemo zinali izi:
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu wanga anaika m'mtima mwanga kuti ndiwasonkhanitse aufulu, ndi olamulira, ndi anthu, kuti awerengedwe mwa chibadwidwe chao. Ndipo ndinapeza buku la chibadwidwe la iwo adakwerako poyamba paja; ndinapeza mudalembedwa m'mwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu wanga anaika m'mtima mwanga kuti ndiwasonkhanitse aufuru, ndi olamulira, ndi anthu, kuti awerengedwe mwa cibadwidwe cao. Ndipo ndinapeza buku la cibadwidwe la iwo adakwerako poyamba paja; ndinapeza mudalembedwa m'mwemo.