Nehemiah 7:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Naŵa anthu a m'chigawo cha Yuda amene adabwerako ku ukapolo, omwe Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adaaŵagwira kupita nawo ku Babiloni. Anthuwo adabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ana a dziko amene anakwera kuchokera kundende a iwo adatengedwa ndende, amene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adawatenga, anabwera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, yense kumudzi wake, ndi awa:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ana a dziko amene anakwera kucokera kundende a iwo adatengedwa ndende, amene Nebukadinezara mfumu ya Babulo adawatenga, anabwera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, yense ku mudzi wace, ndi awa: