Nehemiah 7:61 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ali m'munsiŵa ndiwo amene adabwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adoni ndi ku Imeri, ngakhale sankatha kutsimikiza kuti makolo ao kapena mafuko ao analidi Aisraele enieni kapena ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo okwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, ndi awa; koma sanakhoze kutchula nyumba za makolo ao, kapena mbumba zao, ngati ali a Israele;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo okwera kucokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, ndi awa; koma sanakhoza kuchula nyumba za makolo ao, kapena mbumba zao, ngati ali a Israyeli;