Nehemiah 7:63 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiponso ena mwa ansembe anali aŵa: a banja la Hobaya, a banja la Hakozi, a banja la Barizilai (kunena amene adaakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai wa ku Giliyadi, nkutenga dzina la bambo waoyo).
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi a ansembe: ana a Hobaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana akazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa ndi dzina lao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa: zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi a ansembe: ana a Hobaya, ana a Hokozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana akazi a Barizilai Mgileadi, nachedwa ndi dzina lao.