Nehemiah 7:64 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwoŵa adaafunafuna maina ao m'buku lolongosola kaundula wa mafuko ao, koma maina ao sadapezekemo. Choncho adaŵachotsa pa unsembe naŵaŵerenga kuti ngodetsedwa pa chipembedzo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa chibadwidwe, koma osawapeza; potero anawayesa odetsedwa, nawachotsa kuntchito ya nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa cibadwidwe, koma osawapeza; potero anawayesa odetsedwa, nawacotsa ku nchito ya nsembe.