Nehemiah 7:70 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atsogoleri ena a mabanja adapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa adapereka ku thumba la chuma ndalama zagolide za makilogaramu asanu ndi atatu, mbale makumi asanu, ndiponso mikanjo ya ansembe yokwanira 530.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ena a akulu a nyumba za makolo anapereka kuntchito. Kazembeyo anapereka kuchuma madariki agolide chikwi chimodzi, mbale zowazira makumi asanu, malaya a ansembe makumi atatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ena a akuru a nyumba za makolo anapereka kunchito. Kazembeyo anapereka kucuma madariki agolidi cikwi cimodzi, mbale zawazira makumi asanu, maraya a ansembe makumi atatu.