Nehemiah 7:71 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atsogoleri ena a mabanja adapereka mosungira chumamo ndalama zagolide za makilogaramu 168, ndiponso ndalama zasiliva za makilogaramu 1,250.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Enanso a akulu a nyumba za makolo anapereka kuchuma cha ntchitoyi, madariki agolide zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya mina ya siliva zikwi ziwiri mphambu mazana awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Enanso a akuru a nyumba za makolo anapereka ku cuma ca nchitoyi, madariki agolidi zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya siliva zikwi ziwiri mphambu mazana awiri.