Nehemiah 7:72 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo anthu onse otsala adapereka ndalama zagolide za makilogaramu 168, ndalama zasiliva zamakilogaramu 140, ndiponso mikanjo ya ansembe yokwanira 67.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zopereka za anthu otsala ndizo madariki agolide zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya mina ya siliva zikwi ziwiri, ndi malaya a ansembe makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zopereka za anthu otsala ndizo madariki agolidi zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya siliva zikwi ziwiri, ndi maraya a ansembe makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi awiri.