Nehemiah 7:73 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero ansembe, Alevi, alonda a ku Nyumba ya Mulungu, anthu oimba nyimbo, ambiri mwa anthu wamba, atumiki a m'Nyumba ya Mulungu ndi Aisraele ena onse, ankakhala m'mizinda mwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nakhala m'midzi mwao ansembe, ndi Alevi, ndi odikira, ndi oimbira, ndi anthu ena, ndi Anetini, ndi Aisraele onse. Utakhala tsono mwezi wachisanu ndi chiwiri ana a Israele anakhala m'midzi mwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo. Pofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nakhala m'midzi mwao ansembe, ndi Alevi, ndi odikira, ndi oyimbira, ndi anthu ena, ndi Anetini, ndi Aisrayeli onse. Utakhala tsono mwezi wacisanu ndi ciwiri ana a Israyeli anakhala m'midzi mwao.