Nehemiah 8:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo anthu onse adasonkhana pamodzi pa bwalo la patsogolo pa Chipata cha Madzi. Tsono anthuwo adamuuza Ezara, amene anali mlembi, wansembe ndi mphunzitsi wa malamulo, kuti abwere ndi buku la Malamulo a Mose limene Chauta adaapatsa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi kukhwalala lili ku Chipata cha Madzi, namuuza Ezara mlembi atenge buku la chilamulo cha Mose, chimene Yehova adalamulira Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi pabwalo limene lili patsogolo pa Chipata cha Madzi. Iwo anawuza mlembi Ezara kuti abwere ndi buku la malamulo a Mose limene Yehova anapereka kwa Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi ku khwalala liri ku cipata ca kumadzi, namuuza Ezara mlembi atenge buku la cilamulo ca Mose, cimene Yehova adalamulira Israyeli.