Nehemiah 8:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Alevi adacheteketsa anthu onse naŵauza kuti, “Musalirenso ai, pakuti lero ndi tsiku loyera, choncho musakhale ndi chisoni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Alevi anatontholetsa anthu onse, ndi kuti, Khalani muli chete; pakuti lero ndi lopatulika; musamachita chisoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Alevi anakhalitsa bata anthu onse powawuza kuti, “Khalani chete, pakuti lero ndi tsiku lopatulika ndipo musakhale ndi chisoni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Alevi anatontholetsa anthu onse, ndi kuti, Khalani muli cete; pakuti lero ndi lopatulika; musamacita cisoni.