Nehemiah 8:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo anthu onse adapita kwao kukadya ndi kumwa ndipo zakudya zina adagaŵirako anzao, kuti pakhale chikondwerero chachikulu, chifukwa chakuti tsopano anali atamvetsa bwino mau a Malamulo amene adaaŵerengedwawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Napita anthu onse kudya ndi kumwa, ndi kutumiza magawo, ndi kusekerera kwakukulu; popeza anazindikira mau amene adawafotokozera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onse anachoka kupita kukadya ndi kumwa. Chakudya china anatumiza kwa anzawo. Choncho panali chikondwerero chachikulu popeza tsopano anali atamvetsa bwino mawu a Mulungu amene anawawerengera ndi kuwafotokozerawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Napita anthu onse kudya ndi kumwa, ndi kutumiza magawo, ndi kusekerera kwakukuru; popeza anazindikira mau amene adawafotokozera.