Nehemiah 8:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atsogoleri a mabanja, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, onse adabwera m'maŵa mwake kwa Ezara, mphunzitsi wa malamulo, kuti aphunzire mau a Malamulowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mawa mwake akulu a nyumba za makolo a anthu onse, ansembe, ndi Alevi anasonkhana pamodzi kwa Ezara mlembi, kuti atole nzeru za mau a chilamulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa mwake atsogoleri a mabanja pamodzi ndi ansembe ndi alevi anasonkhana kwa Ezara, mlembi wa malamulo kuti aphunzire mawu a malamulowo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mawa mwace akuru a nyumba za makolo a anthu onse, ansembe, ndi Alevi anasonkhana pamodzi kwa Ezara mlembi, kuti atole nzeru za mau a cilamulo.