Nehemiah 8:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero adafalitsa ndi kulengeza m'midzi yao yonse ndiponso m'Yerusalemu, kuti, “Pitani ku mapiri, mukatengeko nthambi za mtengo wa olivi, za mtengo wa olivi wakuthengo, za mtengo wa mchisu, za mtengo wa mgwalangwa, ndiponso za mitengo ina ya masamba ambiri, kuti mumangire misasa monga momwe zidalembedwera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kuti azilalikira ndi kumveketsa m'midzi mwao monse ndi m'Yerusalemu, ndi kuti, Muzitulukira kuphiri, ndi kutengako nthambi za azitona, ndi nthambi za mitengo yamafuta, ndi nthambi za mitengo yamchisu, ndi zinkhwamba za migwalangwa, ndi nthambi za mitengo zothonana, kumanga nazo misasa monga munalembedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho analengeza ndi kufalitsa mʼmizinda yawo yonse ndi mu Yerusalemu kuti, “Pitani ku phiri mukadule nthambi za mtengo wa olivi, za mtengo wa olivi wa kutchire, za mtengo wa mchisu, za mtengo wa mgwalangwa ndiponso za mitengo ina ya masamba, zomangira zithando monga zalembedweramu ndi kubwera nazo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kuti azilalikira ndi kumveketsa m'midzi mwao monse ndi m'Yerusalemu, ndi kuti, Muziturukira kuphiri, ndi kutengako nthambi za azitona, ndi nthambi za mitengo yamafuta, ndi nthambi za mitengo yamcisu, ndi zinkhwamba za migwalangwa, ndi nthambi za mitengo zothonana, kumanga nazo misasa monga munalembedwa.