Nehemiah 8:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho anthuwo adapita nakatenga zonsezo ndipo aliyense adadzimangira misasa padenga pa nyumba yake, ndiponso m'mabwalo ao, m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu, m'bwalo la pa Chipata cha Madzi ndi m'bwalo la pa Chipata cha Efuremu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natuluka anthu, nakazitenga, nadzimangira misasa, yense pa tsindwi la nyumba yake, ndi m'mabwalo ao, ndi m'mabwalo a nyumba ya Mulungu, ndi pa khwalala la Chipata cha Madzi, ndi pa khwalala la chipata cha Efuremu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anthu anapita kukatenga nthambi ndipo aliyense anadzimangira misasa pa denga ya nyumba yake, mʼmabwalo awo, mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, mʼbwalo la pa Chipata cha Madzi ndiponso mʼbwalo la pa Chipata cha Efereimu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Naturuka anthu, nakazitenga, nadzimangira misasa, yense pa tsindwi la nyumba yace, ndi m'mabwalo ao, ndi m'mabwalo a nyumba ya Mulungu, ndi pa khwalala la cipata ca kumadzi, ndi pa khwalala la cipata ca Efraimu.