Nehemiah 8:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku ndi tsiku kuyambira tsiku loyamba mpaka tsiku lotsiriza, Ezara ankaŵerenga buku la Malamulo a Mulungu. Anthu adachita chikondwerero masiku asanu ndi aŵiri, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu padachitika mwambo wotseka msonkhano, potsata buku la Malamulo lija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anawerenganso m'buku la chilamulo cha Mulungu tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lotsiriza. Nachita chikondwerero masiku asanu ndi awiri; ndi tsiku lachisanu ndi chitatu ndilo msonkhano woletsa, monga mwa malemba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba mpaka lomaliza, Ezara ankawerenga buku la malamulo a Mulungu. Anthu anachita chikondwerero masiku asanu ndi awiri. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu panachitika msonkhano potsata buku la malamulo lija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anawerenganso m'buku la cilamulo ca Mulungu tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lotsiriza. Nacita madyerero masiku asanu ndi awiri; ndi tsiku lacisanu ndi citaru ndilo msonkhano woletsa, monga mwa malemba.