Nehemiah 8:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Ezarayo adabwera ndi buku la Malamulolo, pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, ku msonkhano wa amuna ndi akazi ndi ana amene ankatha kumvetsa zinthu bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ezara wansembe anabwera nacho chilamulo pamaso pa msonkhano, ndiwo amuna ndi akazi, ndi yense wakumva ndi kuzindikira tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri wansembe Ezara, anabwera ndi buku la malamulo ku msonkhano wa amuna, akazi ndi ana onse amene ankatha kumvetsa zinthu bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ezara wansembe anabwera naco cilamulo pamaso pa msonkhano, ndiwo amuna ndi akazi, ndi yense wakumva ndi kuzindikira tsiku loyamba la mwezi wacisanu ndi ciwiri.