Nehemiah 8:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ezara adaŵerenga bukulo atayang'ana bwalo la Chipata cha Madzi, kuyambira m'mamaŵa mpaka pa masana, pamaso pa amuna ndi akazi omwe, ndiponso onse amene ankatha kumvetsa zinthu bwino. Ndipo anthu onsewo ankatchera makutu kuti amve zoŵerengazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nawerenga m'menemo pa khwalala lili ku Chipata cha Madzi kuyambira mbandakucha kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anatcherera khutu buku la chilamulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Ezara anawerenga bukulo atayangʼana bwalo la Chipata cha Madzi kuyambira mmawa mpaka masana pamaso pa amuna, akazi ndi onse amene ankamvetsa bwino zinthu. Ndipo anthu onse anatchera khutu kuti amve malamulowo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nawerenga m'menemo pa khwalala liri ku cipata ca kumadzi kuyambira mbanda kuca kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anacherera khutu buku la cilamulo.