Nehemiah 8:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mlembi Ezara adaaimirira pa nsanja yamitengo, imene anthuwo adaamanga chifukwa cha msonkhanowo. Ku dzanja lake lamanja kudaaimirira Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya ndi Maaseiya. Ku dzanja lake lamanzere kudaaimirira Pedaya, Misaele, Malikiya, Hasumu, Hasibadana, Zekariya ndiponso Mesulamu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ezara mlembi anaima pa chiunda cha mitengo adachimangira msonkhanowo; ndi pambali pake padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseiya, kudzanja lamanja lake; ndi kudzanja lamanzere Pedaya, ndi Misaele, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mlembi Ezara anayimirira pa nsanja ya mitengo imene anthu anamanga chifukwa cha msonkhanowu. Ku dzanja lake lamanja kunayimirira Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya ndi Maaseya, ndipo kudzanja lake lamanzere kunali Pedaya, Misaeli, Malikiya, Hasumu, Hasibadana, Zekariya ndi Mesulamu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ezara mlembi anaima pa ciunda ca mitengo adacimangira msonkhanowo; ndi pambali: pace padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseya, ku dzanja lamanja lace; ndi ku dzanja lamanzere Pedaya, ndi Misayeli, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu.