Nehemiah 9:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudachita zizindikiro ndi zodabwitsa pamaso pa Farao, antchito ake onse, ndi anthu onse okhala m'dziko mwake, popeza kuti mudaadziŵa kuti iwowo adazunza makolo athu. Nchifukwa chake mbiri yanu idakula monga momwe iliri mpaka lero lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nimunachitira zizindikiro ndi zodabwitsa Farao ndi akapolo ake onse, ndi anthu onse a m'dziko lake; popeza munadziwa kuti anawachitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu munachita zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa kutsutsana ndi Farao, pamaso pa Farao, nduna zake ndi anthu onse a mʼdziko lake, pakuti Inu munadziwa kuti anazunza makolo athu. Inu munadzipangira nokha dzina, monga zilili mpaka lero lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nimunacitira zizindikilo ndi zodabwiza Farao ndi akapolo ace onse, ndi anthu onse a m'dziko lace; popeza munadziwa kuti anawacitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino.