Nehemiah 9:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudagaŵa nyanja pakati, anthu anu akupenya, kotero kuti iwowo adaoloka pakati pa nyanja pali pouma. Kenaka mudaŵamiza m'nyanja adani amene ankaŵalondola, monga momwe umachitira mwala m'madzi ozama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu munagawa nyanja anthu anu akupenya, kotero kuti anadutsa powuma, koma munamiza mʼmadzi akuya anthu amene ankawalondola monga mmene uchitira mwala mʼmadzi ozama.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba.