Nehemiah 9:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudaŵapatsa buledi wochokera kumwamba kuti adye. Mudaŵapatsa madzi otuluka m'thanthwe, kuti aphere ludzu. Mudaŵauza kuti apite kukalanda dziko limene Inu mudaalonjeza kuti mudzaŵapatsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi mkate wochokera m'mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi otuluka m'thanthwe munawatulutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene anali ndi njala munawapatsa buledi wochokera kumwamba. Pamene anali ndi ludzu munawapatsa madzi otuluka mʼthanthwe. Munawawuza kuti apite kukalanda dziko limene munalonjeza kuti mudzawapatsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi mkate wocokera m'mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi oturuka m'thanthwe munawaturutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa.