Nehemiah 9:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adakana kumvera, ndipo sankakumbuka zodabwitsa zimene Inu mudaazichita pakati pao. Adakhala okanika, nadzisankhira mtsogoleri woti aŵatsogolere kubwerera ku Ejipito ku dziko laukapolo lija. Koma Inu ndinu Mulungu wokhululuka, wokoma mtima, wachifundo, wosakwiya msanga, wokhala ndi chikondi chachikulu chosasinthika, motero iwowo simudaŵasiye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nakana kumvera, osakumbukiranso zodabwitsa zanu munazichita pakati pao; koma anaumitsa khosi lao, ndipo m'kupanduka kwao anaika mtsogoleri abwerere kunka ku ukapolo wao; koma Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wachisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wochuluka chifundo; ndipo simunawasiya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anakana kumvera ndipo sanakumbukire zodabwitsa zimene munachita pakati pawo. Koma iwo anawumitsa khosi, nakuwukirani podzisankhira okha mtsogoleri kuti awatsogolere kubwerera ku ukapolo ku dziko la Igupto. Koma ndinu Mulungu wokhululukira, wokoma mtima ndi wachifundo wosapsa mtima msanga ndi wachikondi chachikulu chosasinthika. Choncho Inu simunawasiye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nakana kumvera, osakumbukilansozodabwiza zanu munazicita pakati pao; koma anaumitsa khosi lao, ndipo m'kupanduka kwao anaika mtsogoleri abwerere kumka ku ukapolo wao; koma Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wacisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wocuruka cifundo; ndipo simunawasiya.