Nehemiah 9:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele atadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina, adaimirira, nayamba kuulula machimo ao ndi zolakwa za makolo ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nadzipatula a mbumba ya Israele kwa alendo onse, naimirira, nawulula zochimwa zao, ndi mphulupulu za makolo ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeliwa anadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina ndipo anayimirira nayamba kuwulula machimo awo ndi zolakwa za makolo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nadzipatula a mbumba ya Israyeli kwa alendo onse, naimirira, naulula zocimwa zao, ndi mphulupulu za makolo ao.