Nehemiah 9:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudaŵapatsa mphamvu zogonjetsera maiko ndiponso mitundu ya anthu. Mudaŵagaŵiranso maiko achilendo, ndipo choncho adalanda dziko la Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munawapatsanso maufumu, ndi mitundu ya anthu, nimunawagawa m'madera, motero analandira likhale laolao dziko la Sihoni, ndilo dziko la mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu munawapatsa mafumu ndi mayiko mʼmanja mwawo. Munawagawiranso mayiko achilendo akutali kwambiri. Munabwera nawo mʼdziko la Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani kuti alowemo nʼkulitenga kukhala lawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munawapatsanso maufumu, ndi mitundu ya anthu, nimunawagawa m'madera, motero analandira likhale lao lao dziko la Sihoni, ndilo dziko la mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basana.