Nehemiah 9:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho zidzukulu zaozo zidaloŵamo ndi kukhazikika m'menemo, ndipo Inu mukuŵatsogolera, mudagonjetsa Akanani, nzika za m'dzikomo. Akananiwo, ndiye kuti mafumu ao ndi anthu onse am'dzikomo, mudaŵapereka kwa anthu anu, kuti achite nawo monga angafunire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nalowa anawo, nalandira dzikoli likhale laolao, ndipo munagonjetsa pamaso pao okhala m'dziko, ndiwo Akanani, ndi kuwapereka m'dzanja mwao, pamodzi ndi mafumu ao, ndi mitundu ya anthu ya m'dziko, kuti achite nao chifuniro chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho zidzukulu zawo zinapita ndi kukalandira dzikolo. Inu munagonjetsa pamaso pawo, Akanaani amene amakhala mʼdzikolo. Inde munapereka mʼmanja mwawo mafumu awo pamodzi ndi anthu a mʼdzikomo kuti achite nawo monga angafunire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nalowa anawo, nalandira dzikoli likhale lao lao, ndipo munagonjetsa pamaso pao okhala m'dziko, ndiwo Akanani, ndi kuwapereka m'dzanja mwao, pamodzi ndi mafumu ao, ndi mitundu ya anthu ya m'dziko, kuti acite nao cifuniro cao.