Nehemiah 9:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero adagonjetsa mizinda yamalinga nalanda dziko lachonde, nyumba zodzaza ndi zinthu zabwino, zitsime zokumbakumba, minda yamphesa, minda yaolivi ndiponso mitengo yazipatso yochuluka kwambiri. Choncho iwowo ankadya, namakhuta, mpaka kumanenepa, ndipo ankakondwa chifukwa cha ubwino wanu, Inu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo analanda midzi yamalinga, ndi dziko la zonona, nalandira zikhale zaozao nyumba zodzala ndi zokoma zilizonse, zitsime zokumbidwa, minda yampesa, ndi minda ya azitona, ndi mitengo yambiri yazipatso; nadya iwo, nakhuta, nanenepa, nakondwera nako kukoma kwanu kwakukulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo analanda mizinda yotetezedwa ndi dziko lachonde. Anatenganso nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino, zitsime zokumbidwa kale, mitengo ya mphesa, mitengo ya olivi ndi mitengo yambiri ya zipatso. Ndipo anadya nakhuta ndipo anali athanzi. Choncho ankakondwa chifukwa cha ubwino wanu wopambana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo analanda midzi yamalinga, ndi dziko la zonona, nalandira zikhale zao zao nyumba zodza la ndi zokoma ziri zonse, zitsime zokumbidwa, minda yampesa, ndi minda yaazitona, ndi mitengo yambiri yazipatso; nadya iwo, nakhuta, nanenepa, nakondwera nako kukoma kwanu kwakukuru.