Nehemiah 9:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Komabe iwowo sankamvera, ndipo adakuukirani. Adaŵataya kunkhongo Malamulo anu, napha aneneri anu amene ankaŵadzudzula kuti abwerere kwa Inu. Adachita zinthu zoipitsitsa zokunyozani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Komabe iwo anakhala osamvera ndipo anakuwukirani nafulatira malamulo anu. Anapha aneneri anu, amene anakawadandaulira kuti abwerere kwa Inu. Anachita chipongwe choopsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya cilamulo canu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwacitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nacita zopeputsa zazikuru.