Nehemiah 9:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Inu mudaŵapereka kwa adani ao amene ankaŵavuta. Pa nthaŵi imene anali m'mavutoyo, ankalira kwa Inu, ndipo Inu munkaŵamvera muli Kumwambako. Chifukwa cha chifundo chanu chachikulu, mudaŵapatsa atsogoleri amene ankaŵapulumutsa kwa adani ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake munawapereka m'dzanja la adani ao akuwasautsa; koma mu nthawi ya kusautsika kwao anafuula kwa Inu, ndipo munamva m'Mwamba, ndi monga mwa nsoni zanu zambiri munawapatsa apulumutsi akuwapulumutsa m'dzanja la adani ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene anazunzidwa anafuwulira kwa Inu, ndipo Inu munawamvera muli kumwambako. Ndipo mwa chifundo chanu chachikulu munkawapatsa atsogoleri amene ankawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace munawapereka m'dzanja la adani ao akuwasautsa; koma mu nthawi ya kusautsika kwao anapfuula kwa Inu, ndipo munamva m'Mwamba, ndi monga mwa nsoni zanu zambiri munawapatsa apulumutsi akuwapulumutsa m'dzanja la adani ao.