Nehemiah 9:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma atakhala pa mtendere, adayambanso kuchimwa pamaso panu, ndipo mudaŵaperekanso kwa adani ao, kotero kuti adani aowo ankaŵalamulira. Komabe pamene ankabwerera ndi kumalira Inu, Inuyo munkaŵamvera muli Kumwambako. Motero nthaŵi zambiri munkaŵapulumutsa chifukwa cha chifundo chanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma atapumula, anabwereza kuchita choipa pamaso panu; chifukwa chake munawasiya m'dzanja la adani ao amene anachita ufumu pa iwo; koma pobwera iwo ndi kufuula kwa Inu, munamva m'Mwamba ndi kuwapulumutsa kawirikawiri, monga mwa chifundo chanu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma akangokhala pa mtendere ankayambanso kuchita zoyipa pamaso panu. Choncho munkawapereka mʼmanja mwa adani awo amene ankawalamulira. Komabe pamene ankabwerera ndi kumalira kwa Inu, Inu munkawamva muli kumwambako. Chifukwa cha chifundo chanu chochuluka, nthawi zonse munkawapulumutsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma atapumula, anabwereza kucita coipa pamaso panu; cifukwa cace munawasiya m'dzanja la adani ao amene anacita ufumu pa iwo; koma pobwera iwo ndi kupfuula kwa Inu, munamva m'Mwamba ndi kuwapulumutsa kawiri kawiri, monga mwa cifundo canu;