Nehemiah 9:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zoonadi Inu mudaŵachenjeza kuti ayambenso kutsata Malamulo anu. Koma iwo ankadzitukumula, ndipo sankamvera malamulo anu. Adachimwira malangizo anu opatsa moyo kwa anthu oŵasunga. Ankakufulatirani namaumitsa mitu yao, osafuna kumvera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo munawachitira umboni, kuti muwabwezerenso ku chilamulo chanu; koma anachita modzikuza, osamvera malamulo anu; koma anachimwira malamulo anu (amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo); nakaniza phewa lao, naumitsa khosi lao, osamvera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu munkawachenjeza kuti abwerere ndi kuyamba kutsata malamulo anu. Koma iwo ankadzitukumula ndipo sankamvera malamulo anu. Iwo anachimwira malangizo anu amene munati ‘Amapatsa moyo kwa munthu wowamvera.’ Iwo ankakufulatirani, nawumitsa makosi awo osafuna kukumverani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo munawacitira umboni, kuti muwabwezerenso ku cilamulo canu; koma anacita modzikuza, osamvera malamulo anu; koma anacimwira malamulo anu (amene munthu akawacita adzakhala nao ndi moyo); nakaniza phewa lao, naumitsa khosi lao, osamvera.