Nehemiah 9:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nchifukwa chake tsono, Inu Mulungu wathu, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, mumasunga chipangano ndi chikondi chanu chosasinthika. Musalole kuti zosautsa zathu zonse zikuwonekereni ngati zochepa. Zosautsazo zatigwera ife, mafumu athu, akulu athu, ansembe athu, aneneri athu, makolo athu, ndiponso anthu anu onse, kuyambira nthaŵi ya mafumu a ku Asiriya mpaka lero lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsono, Mulungu wathu, ndinu Mulungu wamkulu, ndi wamphamvu, ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo, asachepe pamaso panu mavuto athu onse amene anatigwera ife, ndi mafumu athu, akulu athu, ndi ansembe athu, ndi aneneri athu, ndi makolo athu, ndi anthu anu onse, kuyambira masiku a mafumu a Asiriya, mpaka lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nʼchifukwa chake, tsono, Inu Mulungu wathu, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa kwambiri mumasunga pangano ndi chikondi chosasinthika. Musalole kuti mavuto onse amene atigwera ife, mafumu athu, atsogoleri athu, ansembe athu, aneneri athu, makolo athu ndi anthu ena onse kuyambira nthawi ya mafumu a ku Asiriya mpaka lero aoneke ochepa pamaso panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsono, Mulungu wathu, ndinu Mulungu wamkuru, ndi wamphamvu, ndi woopsa, wakusunga pangano ndi cifundo, asacepe pamaso panu mabvuto athu onse amene anatigwera ife, ndi mafumu athu, akuru athu, ndi ansembe athu, ndi aneneri athu, ndi makolo athu, ndi anthu anu onse, kuyambira masiku a mafumu a Asuri, mpaka lero lino.