Nehemiah 9:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene iwo ankadzilamulira okha, namalandira zabwino zanu m'dziko lalikulu ndi lachonde limene mudaŵapatsa, sadakutumikireni, ndipo sadazisiye ntchito zao zoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza sanatumikire Inu m'ufumu wao, ndi m'ubwino wanu wochuluka umene mudawapatsa, ndi m'dziko lalikulu ndi la zonona mudalipereka pamaso pao, ndipo sanabwerere kuleka ntchito zao zoipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale ankadzilamulira okha, nʼkumalandira zabwino zochuluka mʼdziko lalikulu ndi lachonde limene munawapatsa, koma iwo sanakutumikireni kapena kusiya ntchito zawo zoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza sanatumikira Inu m'ufumu wao, ndi m'ubwino wanu wocuruka umene mudawapatsa, ndi m'dziko lalikuru ndi la zonona mudalipereka pamaso pao, ndipo sanabwerera kuleka nchito zao zoipa.