Nehemiah 9:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano chuma cha dzikolo changolemeza mafumu amene mudaŵaika kuti azitilamulira kaamba ka machimo athu. Ali ndi mphamvu zolamulira matupi athu ndiponso ng'ombe zathu monga afunira. Ndithudi, ife tili m'mavuto aakulu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo lichulukitsira mafumu zipatso zake, ndiwo amene munawaika atiweruze, chifukwa cha zoipa zathu; achitanso ufumu pa matupi athu, ndi pa zoweta zathu, monga umo akonda; ndipo ife tisauka kwakukulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono chifukwa cha machimo athu, mafumu amene munawayika kuti azitilamulira angodzilemeretsa ndi chuma chambiri cha dzikoli. Iwo ali ndi mphamvu zolamulira matupi athu ndi ngʼombe zathu momwe afunira. Zedi, ife tili mʼmavuto aakulu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo licurukitsira mafumu zipatso zace, ndiwo amene munawaika atiweruze, cifukwa ca zoipa zathu; acitanso ufumu pa matupi athu, ndi pa zaweta zathu, monga umo akonda; ndipo ife tisauka kwakukuru.