Nehemiah 9:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa makwerero okhalapo Alevi padaimirira Yesuwa, Bani, Kadimiyele, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani ndi Kenani. Onsewo ankapemphera mokweza mau kwa Chauta, Mulungu wao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anaimirira pa chiunda cha Alevi Yesuwa, ndi Bani, Kadimiyele, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani, ndi Kenani, nafuula ndi mau akulu kwa Yehova Mulungu wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa makwerero okhalapo alevi anayimirirapo anthu awa: Yesuwa, Bani, Kadimieli, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani ndi Kenani. Iwowa ankapemphera mokweza mawu kwa Yehova Mulungu wawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anaimirira pa ciunda ca Alevi Yesuwa, ndi Bani, Kadimiyeli, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani, ndi Kenani, napfuula ndi mau akuru kwa Yehova Mulungu wao.