Nehemiah 9:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Alevi aŵa, Yesuwa, Kadimiyele, Bani, Hasabeniya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya adalengeza kuti, “Imirirani, mumtamande Chauta, Mulungu wanu, nthaŵi zonse. Litamandike dzina lake laulemerero limene anthu sangathe kulilemekeza ndi kulitamanda mokwanira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyele, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petahiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu kunthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa chilemekezo ndi chiyamiko chonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Alevi awa: Yesuwa, Kadimieli, Bani, Hasabaneya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya anati: “Imirirani ndipo mutamande Yehova Mulungu wanu, amene ndi wamuyaya.” “Litamandike dzina lake laulemerero limene liposa madalitso ndi matamando onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyeli, Buni, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petatiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu ku nthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa cilemekezo ndi ciyamiko conse.